Pamene anthu ena akugona ndi njala, ena pa mzere wa mafuta, ndipo mu zipatala mulibe mankhwala, boma latenga ndalama pafupifupi 5 biliyoni ya Malawi kupereka ku kampani ya ku Ghana kuti athane ndi a Bakili Muluzi TV ndi anzawo ena. Kudzera mu bungwe loona zofalitsa nkhani la MACRA, boma lapereka ndalamayi ku kampani ya HASHCOM.
Malinga ndi chikalata chomwe bungwe la MACRA latulutsa, kampani ya ku Ghana iyi ipatsidwa ndalamazi pa ntchito yofufuza nkhani zimene akuti ndi zabodza mu dziko muno.
Ndondomeko imene apelekera ndalamazi ku kampaniyi ikutchedwa “kulondoloza nkhani zabodza ku Malawi” ndipo kampani ya mu dziko la Ghana yayenera kuti ibweretse matchini ndi kuwadzika kuti azitha kulondoloza nkhani zimene a boma akuti ndi zabodza.
Ndalama zimene kampaniyi ipatsidwe ndi zoposa 1.5 miliyoni dollars ya dziko la Amereka imene itasinthidwa pa mtengo wa 3000 Kwacha pa misika ya anthu wamba ikwana 4.5 biliyoni Kwacha ya Malawi.
Katswiri wina wa za kafukufuku wati boma likubisalira chabe konena kuti akufuna kuthana ndi nkhani za bodza. Ati iyi ndi njira yofuna kupeza ndi kuthana ndi anyamata amene akuoneka kuti akhaulitsa boma pa masamba a Mchezo monga a Bakili Muluzi TV.
“Ndalama za nkhani nkhani chonchi akanene kuti ndi chifukwa chofuna kudziwa kayendedwe ka nkhani za bodza? Ili ndi bodza. Alipo andale amene akufuna athane nawo, maka anyamata amene akhala akuwazunguza mutu monga a Bakili Muluzi TV ndi a Limpopo FM,” anatero katswiriyu emwe adakana kumutchula dzina.
Boma lakhala likuvutika kwambiri kuti lithane ndi ofalitsa mawu amene amatchedwa kuti a Bakili Muluzi TV. Nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu kudzanso amene anali nduna ya zam’dziko a Zikhale Ng’oma mmbuyomu adalonjezapo kuti athana nawo anyamatawa koma sizidaphule kanthu.
A Bakili Muluzi TV amagwiritsa ntchito masamba a Intaneti kudzudzula boma. Koma a mbali ya boma amati chabe anyamatawa ndi abodza ndipo ndi ofunika kuthana nawo. Anthu angapo amangidwa mokhudzana ndi tsambali koma sizidaoneke kothera.