Kodi munthu akamayendera galimoto yabwino ndekuti ndi wa Satanic? – Gwamba

Oyimba chamba cha Hip-Hop koma mwauzimu, Gwamba atafunsidwa funso lokuti “Kodi mumakwanitsa bwanji kukhala wa Satanic” nayenso anayankha ndi funso “Kodi munthu akamayendera galimoto yabwino nde kuti ndi wa Satanic?


Anayankhula izi mukucheza kwawo ndi Blesikwa pa kanema yotchewa Pakaya yomwe imawulutsidwa pa tsamba la pa utatavo la Youtube.


Blesikwa anamukanira Gwamba kuti iyeyo sioyankha mafunso koma ofunsa koma sizinaphule kanthu chifukwa oyimba wa Lilongwe-yu adapitiliza kufunsa “iyayi ndifuna ndidziwe mukamati Satanic mumatanthauza chani?


Ngakhale kuti nkhaniyi sinapitilire koma anthu ambiri pa masamba a mchezo maka pa Facebook akhala akumunena Gwamba kuti ndi wa Satanic pa zifukwa zomwe akuzidziwa okha zomwe zinapangitsa Besikwa kuti afunse fusoli.


Ngakhale izi zili chomwecho, anthuwa anakambirana zambiri pakucheza kwawo kuphatikizira mphekesera zomwe zakhala zikumveka kuti Gwamba ndiosamphunzira kamba koti nyimbo zake sagwiritsa ntchito chingerezi ngati oyimba ena a Hip-hop achitira.


“Ndili ndi tsamba la sukulu ya ukachenjede ‘Degree’ ya credit koma sindinagwiritsepo ntchito ndipo sindikudziwa kuti ndinalisiya kuti,” anatero Gwamba mwathamo.


Komatu anatsindika kuti Degree yomwe anapanga ya za malonda imamuthandizira kuyendetsa bwino mbali yayikulu yamayimbidwe ake.


Gwamba anadziwika pafupifupi zaka zoposera khumi zambitazo ndi nyimbo monga ” Ndidikira” “Tikakumane Kumadzi” kungotchula zochepa chabe.


Loweruka likudzali, Gwamba wakhonzanso phwando lamayimbidwe lomwe likutchedwa “The Best of Gwamba Concert” ku bwalo lazamasewero la Civo ku Lilongwe kukondwelera zaka khumi ndi zisanu zamayimbidwe.


Related Articles

Joyah’s short film to stream on Iplus-

Joyah’s short film to stream on Iplus

Award winning filmmaker Shemu Joyah has said his s...

Read More
EU Film Festival 2024 set for 24 October to 2 November-

EU Film Festival 2024 set for 24 October to 2 November

Screening of films for the annual EU Film Festival...

Read More
Euro Film Festival to screen at four venues-

Euro Film Festival to screen at four venues

By Sam Banda Jnr & Jimmy Chazama: The annual Europ...

Read More
Mama my love-

Mama my love

The women were heading in the opposite direction t...

Read More
Temwah Takes the Stage: Award-Winning Artist Named 2024 Ecobank Day Ambassador!-

Temwah Takes the Stage: Award-Winning Artist Named 2024 Ecobank Day Ambassador!

In an exciting announcement, Ecobank Malawi has ap...

Read More