Bungwe loyendetsa mpira la FAM lagamula kuti osewera kutsogolo, Promise Kamwendo abwelere ku team yake ya Dedza Dynamos kamba kakuti mgwirizano omwe osewerayu adasainila ndi team ya Mighty Mukuru Wanderers ngosavomerezeka.

Bungweli lalamuranso osewerayu kubwenza 6 million kwacha yomwe adapochera, yomwe pachingelezi amati ‘signing on fee’ ku team ya Wanderers.

FAM yatinso team ya Dedza Dynamos ibwenze ndalama yokwana 4 million kwacha ku team ya FCB Nyasa Big Bullets yomwe idaperekedwa ngati mgwirizano oti osewerayu apite kumeneku komanso 4 million ku team ya Wanderers.

Dedza Dynamos ayigamulanso kuti ilipire chindapusa cha K3 million kamba kobweretsa mpungwe pungwe ku masewero a mpira wamiyendo.

Nayo Wanderers ayipweteka, team imeneyi ayigamula kuti ilipire chindapusa cha 4 million kamba kophwanya dala malamuro omwe team iliyonse imayenera kutsatira ikamafuna kugula osewera.

Bullets yauzidwanso kuti idalakwitsa ponena kuti Wanderers yatenga osewera wake kamba kakuti pa nthawiyo, mgwirizano udachitika ndi team ya Dedza osati osewera ndipo ichi nchifukwa chake Bullets yalephera kutulutsa umboni owometsa kuti Promise Kamwendo ndi osewera wake.⁴

Bungweli latinso oyimira osewerayu, Hestings Chilunga alibe zipepala zomuyenereza kuti atero ndipo akuyenera kupanga ndondomeko zoyenera kuti bungweli lidzamuvomere kutidi ndi oyenera kuimira osewera.

FAM yaomba mkota ponena kuti osewerayu akabwelera ku Dedza, ma team onsewa ali ndi ufulu tsopano okambilana naye kamba kakuti walowa mu miyezi isanu ndi umodzi omaliza mu mgwirizano wake ndi Dedza ndipo kuti mgwirizanowu udzatha pa 31 December chaka chino.

Bungweli latulutsa chigamulochi potsatira ma umboni onse omwe aperekedwa kuchokera ku mbali zokhudzidwa.

Mwachitsanzo, bungweli lati team ya Dedza, inakana mwa mtu wa galu kuti idalowa mu mgwirizani ndi team ya Wanderers ponena kuti adawauza iwowa kuti sizingathekenso kukambilana za osewerayu kamba kakuti anali atagwirizana kale ndi team ya Bullets.

FAM inatinso potengera ma umboni, zinali zodziwikiratu kuti Dedza ndi Bullets analowa mu mgwirizano ndipo zonse zidatheka malinga ndi momwe malamulo a kugula ndi kugulitsa osewera kamakhalira ndipo zinangotsala kuti osewerayu akasainile mgwirizano watsopano ndi team ya Bullets zomwe sizidachitike kamba kakuti Wanderers idamutenga osewerayu nkukamupatsa kontilakiti.

Bungweli lati yemwe sakukhutira ndi chigamulochi, apange appeal pasanadutse masiku atatu chigamulochi chitatuluka.

Sharing is caring!