Mpondamatiki Elon Musk, yemweso ndi mwini wa tsamba la mchezo la X lija linkachulidwa kuti Twitter, akusambwadzidwa ndi mai wina yemwe anamubelekera mwana koma sakumuthandiza.
Mayiyu yemwe dzina lake ndi Claire Boucher koma amadziwika bwino ndi dzina loti Grimes, walemba pa tsamba la X kumusambitsa chokweza Musk kamba kosathandiza mwana wawo.
Grimes wati wakhala akumuuza Musk kuti athandize mwana wawoyu yemwe pano akudwala, koma bambo wapakhomo pa mwana alirenjiyu sakuchita kanthu zomwe zamupangitsa mayiyu kuvula chinyawu.
Musk ndi mpondamatiki ku America ndipo wakwanitsa kukhala nawo muboma la Donald Trump kamba ka kakukhupuka kwake. Malipoti akusonyeza kuti Musk ndi bambo wosalora siketi idutse. Malingana ndi tsamba la ‘The Standard’, Musk wafesa ana khumi ndi awiri; indee kukwanilitsa malemba.