Katswiri komanso mkhalakale pa uwulutsi wa pa wayilesi, a Lucius Chikuni, amwalira pa chipatala cha Mwaiwathu munzinda wa Blantyre.
Chikuni yemwe amadziwika bwino chifukwa cha mawu ake okhathamira, wamwalira m’bandakucha wa lero Lolemba pa 10 February, 2025.
Kupatula kugwira ntchito ku wailesi za Malawi Broadcasting Corporation (MBC) komanso Zodiak, Chikuni ndi yemwenso adalemba sewero la John Chilembwe (Adaferanji).
Malemu Chikuni omwe adali ochokera ku dera la mfumu yaikulu Chimaliro m’boma la Thyolo, amwalira ali ndi zaka 84.