Skeffa wasintha maganizo, walowa ndale ankati sadzapanga zija

Oyimba Skeffa Chimoto chaka chatha mu January anawuza nyumba yowulutsa mawu ya Times kuti iye alibe chidwi cholowa ndale kutsatila manong’onong’o omwe anamveka atapezeka pa msonkhano wina wachipani cha Malawi Congress (MCP) ku Nkhotakota komwenso ndi kumudzi kwawo. 


Ngakhale kuti dzulo kudzera ku nyumba yomweyi waulura kuti aimira ngati phungu wa nyumba ya malamulo wachipani cha MCP ku dera la kum’mwera chakumvuma kwa boma la Nkhotakota pa chisankho cha chaka chamawa.


“Pressure idachokera kumudzi kwathu komweko ndiye poyamba ndimakana koma nditalingalira ndidadzifunsa kuti bwanji anthu onsewa asankha ine?” anatero Skeffa. 


Koma m’modzi mwa a Katswiri oyankhula pa ndale m’dziko muno George Chaima wati chiganizo cha Skeffa chili ndi zosamwitsa zake ngati munthu komanso oyimba.


“Zikanamveka bwino akanati mtima wake wafuna kuti ayimire dera lakwawo osati anthu anthu achita kumufuna, ukamapanga chinthu choti mwiniwakewe sichinali ku mtima kwako nthawi zambiri zinthu siziyenda. 


penanso anthu amafuna kunamizira kuti anthu achita kuwapepmha pomwe anali kale ndi zolinga,” iye adatero. 


Chaima anafotokozanso kuti Skeffa ngati wayamba ndale ayembekezere kuti zisokoneza luso lake pankhani yamayimbidwe. 


“Taonapo oyimba ngati Allan Ngumuya, Billy Kaunda komanso malemu Lucius Banda mbali yawo yamayimbidwe inalowa pansi atalowa ndale, mwachitsanzo munthu sungatumikire ambuye awiri,” adawonjezera kufotokoza. 


Mu chakachi mwa oyimba ena awonetsapo chidwi kupanga nawo ndale ndi monga Fredokiss ndi Anne Matumbi.


Related Articles

Chambiecco’s new Amapiano Jam leaves dancehall fans scratching their heads-

Chambiecco’s new Amapiano Jam leaves dancehall fans scratching their heads

In the ever-evolving landscape of music, the relea...

Read More
Unima lecturer to launch poetry book-

Unima lecturer to launch poetry book

University of Malawi (Unima) Associate Professor i...

Read More
Great Angels Choir hits Amapiano: Did they leave their harmony at home?-

Great Angels Choir hits Amapiano: Did they leave their harmony at home?

The Great Angels Choir's contribution to the new g...

Read More
Joyous Celebration crew starts jetting in-

Joyous Celebration crew starts jetting in

By Jimmy Chazama Members of South African gospel m...

Read More
Onesimus wins sixth award, capping off an impressive year-

Onesimus wins sixth award, capping off an impressive year

Malawian musician Onesimus has added another feath...

Read More
Crisis libation in BT City-

Crisis libation in BT City

Lost History Foundation, in partnership with Chipe...

Read More